Menya ubuzima, kwizera n’ibisobanuro
Kodi Alpha ndi chani?
Alpha ndi ndondomeko zamaphunziro ofuna kuunikira moyo wa chikhristu. Chilichonse chomwe timakambirana chimayima pa mutu wa chikhulupiliro ndipo pamakhala mafunso omwe amathandizira kuti pakhale kukambirana. Alpha imapezeka mayiko onse ndipo aliyense ndi olandiridwa kutenga nawo gawo. Alpha imayendetsedwa kudzera pa intaneti, mu malo ochezera, mu matchalitchi, mu masukulu aukachenjede, kunyumba komanso malo ena ambiri. Maphunziro a Alpha alipo osiyanasiyana koma pali zinthu zitatu zomwe ndizofanana ndipo ndi zinthu ngati: kucheleza alendo, zokambirana komanso kucheza kwabwino.

Maphunziro a Alpha amawoneka motani?

Kulumikizana
Kaya mukudya limodzi penapake, kapena mukulankhulana pogwiritsa ntchito njira zamakono monga foni, aliyense ali ndi kapu yake ya tiyi m’manja, maphunziro onse a Alpha amayamba ndi kudziwana, kuchezerana komanso kumanga ubale. Kudyera limodzi kuli ndi kuthekera kothandizira anthu kuti achezerane momasuka ndi kudziwana bwino bwino kuposera kale.

Kuwonelera
Maphunziro a Alpha amaluzanitsa anthu osiyanasiyana kubwera pamodzi ndikuyamba kugawana nzeru. Anthuwa, amayamba kukambirana zinthu zikulu zikulu zokhudza moyo komanso zinthu zofunikira pa nkhani ya kukhulupilira mwa Khristu, mafunso monga “Kodi Yesu ndi ndani?” komanso “Kodi Mulungu amatitsogolera bwanji?”

Kukambirana
Iyi imakhala nthawi yoti anthu apereke maganizo awo, amve maganizo a anthu ena komanso kuti alankhulepo momwe iwo akuwonera kuchokera pansi pamtima wawo ndipo zonsezi zimayenera kuchitika mwachikondi komanso momasuka.
Onerani zokambirana za Alpha
Alpha Youth Talks Africa (makanema a achinyamata koma otanthauziridwa mu chilankhulo cha dziko la Rwanda
Makanema a zokambirana za Alpha za a achinyamata, amapereka mpata kwa achinyamata kuti athe kufunsa mafunso ozama okhudza moyo, chikhulupiliro komanso Mulungu.
Mu maphunziro a Alpha muli nkhani zochititsa chidwi, muli zithunzi, muli mafunso, komanso fundo zotsogolera pa zokambirana, ndipo izi zimathandzira achinyamata kulingalira kuti zinthu zonsezi zikukhudza bwanji moyo wawo, ndipo iwo amakhala ndi mwayi okambirana ndi anzawo komanso a dindo.
Ndingayambe bwanji?
IChilichonse chofunikira pa maphunziro a Alpha chikupezeka pa intaneti ndipo ndi za ulere kotero kuti aliyense akhoza kutenga nawo gawo posintha miyoyo.
Pa ‘MyAlpha’ ndipomwe muyambire kukonzekera maphunziro anu a Alpha; pamenepa mukapeza zonse kuyambira zomwe mukuyenera kuphunzira, zipangizo zokuthandizirani kuphunzira, mauthenga olengezetsera komanso maphunziro ojambulidwa pa kanema.

Konzekerani maphunziro anu a Alpha
Lembetsani maphunziro anu a Alpha kuti muthe kugawa bwino nthawi yophunzilira ndi gulu lanu, kugawa ziphunzitso komanso kudziwa nthawi yomwe mukhale mwayima kupanga maphunziro a Alpha. Kudzera mu ‘MyAlpha’ muthanso kupereka mwayi ku gulu lanu kuti lithe kupeza mauthenga ndi zipangizo zonse zolengezetsera maphunziro anu a Alpha. Onesetsani kuti mukulengezetsa za a Alpha ndi cholinga choti uthengawu ufikire anthu ambiri.

Phunzitsani gulu lanu
Mumaphunzirowa muli makanema omwe ali ndi upangili okwana kwa inu komanso ndi gulu lanu pofuna kuthandizirani kuti mukayendetse bwino maphunziro a Alpha. Maphunzirowa anayikidwa mumagawo magawo ovomerezeka oyendetsera maphunziro a Alpha mumadera onse, kuyambira kwa a chinyamata kufikira kwa m’khristu ovomerezeka, kufikira kuti tsopano ndiwe okonzeka kupambana.

Lengezetsani maphunziro anu a Alpha
Mauthenga onse apakanena ndi zina zonse zokuthandizirani kulengezetsa Alpha yanu akupezeka mwaulere mukapita pomwe pali mau oti “Promote” kuti mulengezetse maphunzirowa mu mipingo mwanu, mumadera mwanu komanso pa masamba a mchezo. Osayiwala kulimbikitsa omwe mumasonkhana nawo limodzi kuti akayitanire anzawo.

Konzekerani maphunziro oyamba
Pofuna kukonzekera maphunziro a Alpha, pitani pomwe pali mawu oti ‘What’s next’ kapena mawu oti ‘Series Materials’ pomwe mukapeze makanema komanso mauthenga olembedwa ndi ndondomeko zomwe mungatsatire pa zokambirana pa gulu lanu ndi alendo omwe mwawaitana. Zabwino zonse, apa tsopano mwakonzeka kuyamba maphunziro a Alpha.

Buku loyendetsera Alpha: Zonse zili momwemu
Tatolera ndi kuyika pamodzi zofunikira zonse zokuthandizirani inu pa maphunziro a Alpha. Pezani bukuli ndi zina zambiri mwaulere pa ‘MyAlpha’ kudzera pa makina a intaneti.
Uthenga wabwino ndi waulere – chomwechonso Alpha
